Nikāh yopanda ankhoswe
Download PDFLero ndi: Wednesday, Safar 11, 1447 12:09 AM | Omwe awerengapo: 253
Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
Kuti nikāh itheke, pakuyenera kukhala zinthu zinayi: walī, kugwirizana nako komwe mwamuna wachita, kuvomereza komwe mkazi wachita, ndi mboni ziwiri. Umboni wa izi tikuupeza mu hadīth ya Ibn ‘Abbās:[1]
فَالنِّكَاحُ يَثْبُتُ بِأَرْبَعَةِ أَشْيَاءَ الْوَلِيُّ وَرِضَا الْمَنْكُوحَةِ وَرِضَا النَّاكِحِ وَشَاهِدَيْ عَدْلٍ.
“Tsopano nikāh imatheka kudzera mu zinthu zinayi izi: walī, kukondwera kwa wokwatibwa, kukondwera kwa wokwatira, komanso mboni ziwiri zachilungamo.”
Tikaona mu hadīth ya ‘Ā`ishah, Ibn ‘Abbās ndi ‘Imrān Ibn Huswayn, Mtumiki (ﷺ) akufotokoza kuti:[2]
لَا نِكَاحَ إلَّا بِوَلِيٍّ وَشَاهِدَيْ عَدْلٍ وَمَا كَانَ مِنْ نِكَاحٍ عَلَى غَيْرِ ذَلِكَ فَهُوَ بَاطِلٌ.
“Palibe nikāh ngati palibe walī komanso mboni ziwiri zachilungamo. Ndipo nikāh yomwe siikupezeka chimodzi mwa ziwirizi, imeneyo siyovomerezeka.”
Imām Ash-Shāfi’ī adati:[3]
فَإِنَّ أَكْثَرَ أَهْلِ الْعِلْمِ يَقُولُ الْفَرْقُ بَيْنَ النِّكَاحِ وَالسِّفَاحِ الشُّهُودُ.
Ndithudi ochuluka mu gulu la ma Ulamā (ophunzira akuluakulu a chisilamu) adati: “Kusiyana kwa An-Nikāh ndi As-Sifāh (chibwenzi) ndiye ndi kupezeka kwa mboniku.”
Mu kufotokoza kwake Ibn Qudāmah akuti:[4]
أنَّه لا يَنْعَقِدُ إلَّا بشَهادةِ مُسْلِمَيْنِ، سواءٌ كان الزَّوْجانِ مُسْلِمَيْنِ، أو الزَّوْجُ وَحْدَه.
Ukwati ukuyenera kuchitika pokhapokha ngati pali mboni ziwiri za chisilamu, kaya okwatiranawo onse ndi asilamu kapane mwamuna yekha ndi msilamu.
As-Sarkhasī akuyankhula kuti:[5]
النِّكَاحَ عَقْدٌ عَظِيمٌ خَطَرُهُ كَبِيرٌ، وَمَقَاصِدُهُ شَرِيفَةٌ وَلِهَذَا أَظْهَرَ الشَّرْعُ خَطَرَهُ بِاشْتِرَاطِ الشَّاهِدَيْنِ فِيهِ مِنْ بَيْنَ سَائِرِ الْمُعَاوَضَاتِ.
Nikāh ndi chinthu chofunikira kwambiri (mchisilamu), ndipo zolinga zake ndi zolungama. Choncho, chisilamu chimaphunzitsa kuti payenera kukhala mboni ziwiri kuti ukwatiwu utheke, kusiyana ndi migwirizano ina yonse.
Tikati mboni ziwiri apa sitikunena ankhoswe. Tikamati ankhoswe, tikutanthauza amuna awiri – m’modzi wochokera mbali ya kwa mwamuna ndipo winayo wochokera mbali ya kwa mkazi – omwe amagwira ntchito yoyanjanitsa awiriwa pakati pawo pakakhala kusamvana. Koma anthu amenewa sakuyenera kusankhidwiratu nikāh isanachitike. Izi zikutsutsana ndi malangizo a Allāh pa nkhaniyi:[6]
وَإِنْ خِفْتُمْ شِقَاقَ بَيْنِهِمَا فَابْعَثُوا حَكَمًا مِّنْ أَهْلِهِۦ وَحَكَمًا مِّنْ أَهْلِهَآ إِن يُرِيدَآ إِصْلَاحًا يُوَفِّقِ اللَّهُ بَيْنَهُمَآۗ إِنَّ اللَّهَ كَانَ عَلِيمًا خَبِيرًا
Ndipo ngati mukuopa kusemphana pakati pa awiriwa (mwamuna ndi mkazi); tumizani nkhoswe kuchokera ku banja la mwamunayo komanso nkhoswe kuchokera ku banja la mkazi. Ngati awiriwa akufuna kukonza zinthu pakati pawo; Allāh adzakwaniritsira zimenezo pakati pawopo. Ndithudi, Allāh ndi Wodziwa komanso Wakutha kufotokoza.
Ibn Kathīr adachitira ndemanga pa āyah imeneyi kuti:
وقال الْفُقَهَاءُ: إِذَا وَقَعَ الشِّقَاقُ بَيْنَ الزَّوْجَيْنِ، أَسْكَنَهُمَا الْحَاكِمُ إِلَى جَنْبِ ثِقَةٍ، يَنْظُرُ فِي أَمْرِهِمَا وَيَمْنَعُ الظَّالِمَ مِنْهُمَا مِنَ الظُّلْمِ. فَإِنْ تَفَاقَمَ أَمْرُهُمَا وَطَالَتْ خُصُومَتُهُمَا، بَعَثَ الْحَاكِمُ ثِقَةً مِنْ أَهْلِ الْمَرْأَةِ وَثِقَةً مِنْ قَوْمِ الرَّجُلِ، لِيَجْتَمِعَا فينظرا فِي أَمْرِهِمَا وَيَفْعَلَا مَا فِيهِ الْمَصْلَحَةُ، مِمَّا يَرَيَانِهِ مِنَ التَّفْرِيقِ أَوِ التَّوْفِيقِ، وتشوَّف الشَّارِعُ إلى التوفيق، ولهذا قال تَعَالَى: {إِنْ يُرِيدَآ إِصْلَاحاً يُوَفِّقِ اللَّهُ بَيْنَهُمَآ}.
Adayankhula ma fuqahā’ kuti: pamene kusagwirizana kwabwera pakati pa mwamuna ndi mkazi a pa banja; wogamula milandu amawadekhetsa powalozera kwa munthu wodalirika amene ataunike nkhani ya awiriwo ndipo amamuletsa uyo amene akufuna kupondereza mnzake kuti asapondereze. Ngati nkhani yawoyi ikuoneka kuti ikupitirirabe ndipo zinthu sizili bwino pakati pawo, wogamula milandu amatumiza mwamuna wodalirika kuchokera ku banja la mkazi komanso wodalirika kuchokera banja la mwamuna; yemwe atawakhazike awiriwa pansi ndi kuunika nkhani yawoyi ndi kuchita m’menemo zoyenerera kumbali yoti kodi awiriwa akhalire limodzi kapena asiyane – ndipo Wopereka malamulo (Allāh) wasankha kukhalira limodzi ngati chinthu chabwino pamene akuyankhula kuti: {Ngati awiriwa akufuna kukonza zinthu pakati pawo; Allāh adzakwaniritsira zimenezo pakati pawopo}
Kuchokera mu āyah imeneyi komanso ndemanga imeneyi, zikuonetsa kuti ankhoswewa sakufunikira pamene nikāh ikuchitika. Iwowo amafunikira pamene pabwera kusamvana pakati pa mwamuna ndi mkazi basi. Ndipo tikamumvetsetsa Allāh mu kuyankhula kwake, zikuonetsa kuti anthuwa amachita kusankhidwa. Si anthu oti alipo kale achikhalire ngati m’mene ma kuffar ndi ena osazindikira mu gulu la asilamu adakhazikitsira pakati pawo.
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.
[1] Kitāb Al-Umm la Imām Ash-Shāfi’ī, Vol. 5, tsamba 180
[2] Muswannaf ‘Abdur-Razzāq, Vol. 6, tsamba 266, hadīth #11317; Ibn Hibbān, #4075; Ad-Dāraqutnī, #3521
[3] Kitāb Al-Umm la Imām Ash-Shāfi’ī, Vol. 5, tsamba 180
[4] Al-Mughniy, Vol. 7, tsamba 9
[5] Al-Mabsūtw, Vol. 5, tsamba 11
[6] Sūrah An-Nisā’ 4:35