Kudzichekera mankhwala achikuda

Download PDF

Lero ndi: Wednesday, Safar 11, 1447 12:05 AM | Omwe awerengapo: 263

Funso:

02 August, 2025

As-Salam alaykum! Kodi munthu woti unadzichekera mankwala achikuda mosadziwa malamulo achisilamu, ndiye kutha kwa nthawi wazindikira kuti ndi haram, ungatani?

Yankho:

Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
 
Choyamba, munthu azindikire kuti kuchekera mankhwala achikuda kumagwera mu zigawo ziwiri. Gawo loyamba lili pawiri: kudzera mu njira yoletsedwa yomwe ndi kupita kwa sing’anga, wamatalasimu, wamaula, mfiti kapena mlosi. Kapena kudzera mu njira yololedwa yomwe ndi kuchekeredwa ndi wodziwa zitsamba amene sakugwera mu gulu loyambalo.
 
Ngati munthu unadzichekera mankhwala amene unakatenga kwa anthu a gulu loyambalo, pamenepo ukuyenera kulapa kwa Allāh chifukwa unapita ku malo oletsedwa. Abī Hurayrah akufotokoza kuti Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adati:[1]
 
مَنْ أَتَى سَاحِرًا، أَوْ ‌كَاهِنًا، أَوْ عَرَّافًا، فَصَدَّقَهُ بِمَا يَقُولُ فَقَدْ بَرِئَ ‌مِمَّا ‌أُنْزِلَ عَلَى مُحَمَّدٍ صَلَّى اللهُ عَلَيْهِ وَسَلَّمَ.
 
Aliyense amene wapita kwa Mfiti, kapena Bimbi, kapena Wamaula kenako nakhulupirira zomwe wayankhula iyeyo; pamenepo basi wakanira mu zomwe zidavumbulutsidwa kwa Muhammad (ﷺ).
 
Gawo lachiwiri ndi mtundu wa mankhwala omwe ukuchekeredwawo kuchokera kwa munthu wa gulu lachiwirilo. Mtundu woyamba ndi mankhwala amene ali oletsedwa monga: mankhwala a mwayi, mangolomera, odzitetezera ku ufiti ndi matsenga kapena mankhwala alionse omwe akugwera mu zoterezi.
 
Jābir Ibn ‘Abdullāh akufotokoza kuti:[2]
 
سُئِلَ رَسُولُ اللَّهِ صَلَّى اللهُ عَلَيْهِ وَسَلَّمَ عَنِ النُّشْرَةِ، فَقَالَ: هُوَ مِنْ عَمَلِ الشَّيْطَانِ.
 
Mtumiki wa Allāh (ﷺ) adafunsidwa zokhudza kupeza machiritso kudzera mu ufiti (An-Nushrah), choncho iye adati: “Imeneyo ndi imodzi mu ntchito za Shaytwān.”
 
Mtundu wachiwiri ndi mankhwala amene ali ololedwa ndipo ndi odziwika kuti Allāh adaikamo machilitso pa nthenda imene ukufuna kuti uchireyo. Monga mankhwala a mutu wa ching’alang’ala, mankhwala a mphumu, ndi ena oterowo omwe munthu umathanso kuwapeza kudzera ku chipatala.
 
Usāmah Ibn Sharīk adafotokoza kuti:[3]
 
قَالَتِ الأَعْرَابُ: يَا رَسُولَ اللَّهِ! أَلاَ نَتَدَاوَى؟ قَالَ:‏ نَعَمْ يَا عِبَادَ اللَّهِ! تَدَاوَوْا، فَإِنَّ اللَّهَ لَمْ يَضَعْ دَاءً إِلاَّ وَضَعَ لَهُ شِفَاءً أَوْ قَالَ دَوَاءً إِلاَّ دَاءً وَاحِدًا‏.‏ قَالُوا: يَا رَسُولَ اللَّهِ وَمَا هُوَ؟ قَالَ:‏ الْهَرَمُ.‏
 
Adayankhula munthu wachiluya wochokera kumudzi kuti: Eh iwe Mtumiki wa Allāh (ﷺ)! Kodi tidzisakasaka mankhwala (kuti tipezemo machilitso)? Iye adati: “Eya, eh inu akapolo a Allāh! Sakanisakani machilitso. Chifukwa Allāh sanabweretse nthenda kupatula kuti anaiikiranso machilitso, kapena anati: mankhwala; kupatulapo nthenda imodzi.” Iwo adati: Eh iwe Mtumiki wa Allāh (ﷺ)! Kodi nthenda imeneyo ndiye it? Iye adati: “Imfa.”
 
Kusonyeza kuti kusakasaka mankhwala mu njira yololedwa ndi zovomerezeka mu chisilamumu.
 
Tsopano kwa uyo amene wapeza mankhwala kudzera mu njira ya harām, ameneyo alape kwa Allāh ndipo asadzabwererenso ku ntchito imeneyi.
 
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.


[1] Musnad Ibn Al-Ja’d, #1951, Musnad Ahmad, #9288


[2] Sunan Abī Dāwūd, #3868


[3] Sunan at-Tirmidhī, #2038

Funsoli lakuthandizani?