Kodi afiti ali ndi mphamvu zovulaza munthu?
Download PDFLero ndi: Wednesday, Safar 11, 1447 5:56 PM | Omwe awerengapo: 452
Kodi afiti aja ali ndi mphamvu yopeleka nthenda kwa munthu? Ngati ndi ayi, zimatheka bwanji kut iwowo azipanga matsenga awowo kulodza munthu? Ngati eya, mphamvuzo amazitenga kuti?
Kutamandidwa konse ndi kwa Allāh!
Choyamba, Allāh akuyankhulapo zokhudza afiti motere:[1]
وَمَا هُم بِضَآرِّينَ بِهِ مِنْ أَحَدٍ إِلَّا بِإِذْنِ اللَّهِ.
Koma iwowo savulaza aliyense kudzera mu iwo (ufitiwo) kupatulapo mu chilolezo cha Allāh.
Ibn Kathīr ndi Abī Hātim adafotokoza kuti:[2]
قَالَ سُفْيَانُ الثَّوْرِيُّ: إلا بِقَضَاءِ اللَّهِ، وقال الحسن البصري: مَنْ شَاءَ اللَّهُ سَلَّطَهُمْ عَلَيْهِ وَمَنْ لَمْ يَشَأِ اللَّهُ لَمْ يُسَلِّطْ، وَلا يَسْتَطِيعُونَ ضَرَّ أَحَدٍ إِلا بِإِذْنِ اللَّهِ.
Adayankhula Sufyān Ath-Thawrī: “Kupatulapo mu chilamulo cha Allāh.” Ndipo Al-Hasan Al-Baswrī adati: “Yemwe Allāh wamufuna (kuti ufitiwo umugwere), amawapangitsa iwowo (afitiwo) kumuchita zomwe akonzazo. Ndipo yemwe Allāh sadamufuna (kuti usamugwere), iwowo sakwanitsa. Ndipo afiti sabweretsa vuto pa aliyense kupatulapo kudzera mu chilolezo cha Allāh.”
Ibn Is-hāq adati:[3]
أَيْ بِتَخْلِيَةِ اللَّهِ بَيْنَهُ وَبَيْنَ مَا أَرَادَ.
Kutanthauza kuti: “Kusiidwa kumene Allāh amachita pakati pa iyeyo (wouchita ufitiwo) ndi zomwe Allāh wafuna.”
Mu gawo limene adayankhula Ibn Is-hāq tipezamo zinthu zitatu:[4]
1. Zita kutanthauza kuti Allāh Wapamwambamwamba amamusiya mfitiyo kuti achite za matsengazo. Ndipo akadafuna Allāh sakanatha kukwanitsa zimenezo ndipo sakadatha kumulodza aliyense kuchokera mu chilengedwe Chake.
2. Kapena zitha kutanthauza kuti: “Kudzera mu chikonzero cha Allāh (Qadar Yake).” Ngati momwe adayankhulira Sufyān Ath-Thawrī.
3. Kapena zitha kutanthauza kuti: Iwowo sasocheretsa (ndi ufiti wawowo) kupatulapo amene Allāh akuwadziwa kuti zidzawachitikira zimenezo mu chikonzero Chake. Izi adayankhula ndi Ibn ‘‘Abbās.
Pa chifukwa ichi, mfiti aliyense alibe mphamvu yobweretsa vuto kwa wina aliyense. Ngati zomwe iyeyo wakonza zamuvulaza wina wake, zimenezo ndi zomwe Allāh waloleza kudzera mu uzindikiri Wake komanso chikonzero Chake. Ndipo yemwe ufitiwo sudamufikire, ameneyo watetezedwa ndi Allāh kudzeranso mu chikonzero Chake.
Choncho, ufiti suvulaza aliyense kupatulapo yemwe akuuchitayo. Chifukwa ena omwe akupangiridwa ufitiwo amakhala kuti akudutsa mu zimene Allāh wawakonzera. Iwowo akhonza kutetezedwa ndi Allāh, kapena Allāh akhonza kuwasiya kuti uwagwere ndi cholinga choti apirire ndi kulandira malipiro ochuluka kuchokera kwa Allāh ngati ali okhulupirira.
Adayankhula Al-Hasan Al-Baswrī kuti:[5]
لَا يَضُرُّ هَذَا السِّحْرُ إِلا مَنْ دَخَلَ فِيهِ.
Suvulaza ufiti umenewu kupatulapo amene waulowa (amene amauchita).
Allāh ndiye Mwini kuzindikira.
[1] Sūrah Al-Baqarah 2:102
[2] Tafsīr Ibn Kathīr, Vol. 1, tsamba 364; Tafsīr Ibn Abī Hatim, Vol. 1, tsamba 193, 194
[3] Tafsīr Ibn Abī Hatim, Vol. 1, tsamba 193
[4] Al-Kifāyah fi At-Tafsīr bil Ma’thūr, Vol. 3, tsamba 69
[5] Tafsīr Ibn Abī Hatim, Vol. 1, tsamba 193